Christian Hope Association
205 South B.C. Avenue, Suite #105, Lynden, Washington 98264
Phone: 360-354-HOPE   Fax: 360-354-0623

“Offering Hope at the point of need with a view to Help them succeed”

For over 35 years, the Christian Hope Association has been faithfully serving north Whatcom County communities with a variety of basic human social service needs.

Introduction Translations Notes Study Guide Home

Apostles Creed Study Guide in Chichewa

Phunziro la Chikhulupiliro cha Apositoli mu Chichewa

Chikhulupiliro cha Apositoli sinthambi ya baibulo, koma ndi uthenga wa maphunziro a tchalichi cha Akhrisitu. Mawu adzibvomerezi khumi ndi ziwiri a choonadi analembedwa zaka mazana ndi mazana apitawo, koma alibe ndi tathauzo lodzichepetsa, kuwala ndi choonadi.

Tiphunzira mawu onse ndi ndime za m'baibulo ndi mafunso. Mungaphunzire mapeji otsatilawa pa nokha kapena kuphunzila pokambilana mu magulu.

I. Ndikhulupilira Atate Mulungu Mlengi wakumwamba ndi dziko lapansi.

1. Werengani nkhani ya chilengedwe mu Genesesi ndime yoyamba ndi yachiwiri.

2. Werengani mau a Mulungu kwa a Isilayeli muYesaya 40:6-31.

3. Werengani za m'mene Mulungu anayakhira za makayiko a mwana wa Mulungu m'bukhu la Ntchito ndime 38-41.

4. Werengani m'mene Mulungu aliri ndi anthu amene samamupembeza ngati mlengi m'bukhu la Aroma 1:18-25.

Mafunso:

1. Genesesi ndi bukhu lotsabvuta, anthu achikhulupiliro chochepa angalimvetse. Nanga ndi chifukwa chiyani anthu ena samabvomeleza nkhani ya chilengedwe? Werenganinso Akorinto oyamba 1:18-31.

2. Poti Mulungu ndi wamkulu wamphamvu, wodzidalira, ndi chifukwa chiyani amadandaula za anthu? Onaninso bukhu la Petro oyamba 3:8-10.

3. Tikatenga bukhu la Ntchito ngati chitsanzo cha maweluzo a chikhalidwe, tingagwirizane nadzo, kapena kukambirana ndikufunsana, kapena kunyoza? Werengani Ntchito ndime yoyamba ndi yachiwiri. Werenganinso 2:9-10.

4. Kodi ndi tchimo lanji liri mu ndime imeneyi nanga Mulungu wachita chiyani?

Mayankho:

1. _____________________________________________________

_______________________________________________________

2. _____________________________________________________

________________________________________________________

3. _____________________________________________________

_______________________________________________________

4. _____________________________________________________

_______________________________________________________

II. Ndi mwa Yesu Khrisitu, Mwana wake yekha, wa Atate athu.

1. Werengani m'mene kubadwa kwa Yesu kunalembedwela m'bukhu la Luka 1:26-38 ndi m'mene anaukila kwa akufa m'bukhu la Luka 2:1-20.

2. Werengani m'mene Yesu anenera za chigwirizano chake ndi Mulungu Atate m'bukhu la Yohane 20:17 ndiponso

mavesi 28-29.

3. Werengani Aroma 8:1-4 kuti muone chikondi cha Mulungu Atate ndi Mwana wake Yesu Khrisitu.

4. Werengani Yohane 1:1-5 za ulemelero wakumwamba wa Yesu.

Mafunso:

1. Onani m'mene analembera ndime ya Mika 5:2 zaka mazana apitawo Yesu asanabadwe ndi nkhani ya m'chipangano chatsopano.

2. Ndi lonjezo lotani limene Yesu analonjeza omubvomela ngati mpulumutsi ndi mtsogoleri wao?

3. Kodi vesi 3 limatiuza bwanji kuti Yesu ndi ndani ndipo ndi chifukwa chiyani anabwera pa dziko lapansi?

4. Nanga ndime imenenyi imatiuza bwanji za kufana kwa Atate ndi Mwana?

Mayankho:

1. _____________________________________________________

_______________________________________________________

2. _____________________________________________________

________________________________________________________

3. _____________________________________________________

_______________________________________________________

4. _____________________________________________________

_______________________________________________________

III. Kudzera Mumzimu Woyera, anabadwa kwa mai Maria.

1. Werengani zimene Mateyu woyera ananena poonjezera nkhani ya Luka za kubadwa kwa Yesu mu Mateyu 1:18-25.

2. Werengani Ahebri 4:14-15 ndi Luka 2:41-52 m'mene Yesu anakhalira pa dziko lapansi ngati mwana wa Mulungu.

3. Werengani Yesaya 9:6-7 ndi Yesaya 7:13-14 kuti muone zimene Chipangano Chakale chimanena zakubadwa kwa Yesu ndi momwe zinaonekera mu Chipangano Chatsopano.

4. Werengani mavesi 17-23 a Ayuda kuti muone mphamvu ya mzimu woyera my moyo wa Akhrisitu.

Mafunso:

1. Kodi Yosefe ankafuna kutani atadzindikira kuti Maria ndiwodwala, nanaga anachita chiyani?

2. Muli ndi maganizo anji podzindikira kuti Yesu ndi mtumiki wathu kwa Atate, ndiponso kuti anakhala padziko lapansi ndimabvuto ngati a inu ndi ine.

3. Kodi ndi chifukwa chiyani kubadwa kwa Yesu kudzera mu mzimu woyera kuli kofunika kwa Akhrisitu?

4. Nanga ngati Akhrisitu tiyenera kutani?

Mayankho:

1. _____________________________________________________

_______________________________________________________

2. _____________________________________________________

________________________________________________________

3. _____________________________________________________

_______________________________________________________

4. _____________________________________________________

_______________________________________________________

IV. Anadzudzidwa ndi Apolinto Pilato, anakhomedwa pa mtanda, nafa ndi kuikidwa m'manda, ndikukhala ndi akufa.

1. Werengani za kugwidwa, Kuyimbidwa mlandu, kukhomedwa pa mtanda ndi kuikidwa m'manda kwa Yesu mu Yohane ndime 18 ndi19.

2. Werengani Mateyu 26:52-54 kuti mudziwe m'chifukwa chiyani Yesu sanachite chiri chonse.

3. Werengani Ahebri 2:14-17 kuti mumvetse chifukwa chake Yesu anayera Kufa.

4. Werengani m'bukhu la Mateyu 27:45-46 ndi Luka 22:39-44 za m'mene Yesu anadzudzikira pototsedwa ndipo Atate anamusiya yekha.

Mafunso:

1. Kodi Yesu anachimwa chiyani? Nanga anadzudzikira chiyani? (Nanga ndi machimo andani amene anadzudzikira?)

2. Werenganinso Yohane 12:27 kuti muone kudzipereka kwake. Nanga ndichifukwa chiyani anabwera pa dziko lapansi?

3. Kodi womutsatira Abulahamu anali ndani mu Ahebri 2:16 nanga m'chifukwa chiyani imfa inayeneleka?

4. Kodi zina kutotsedwa kwa Yesu ndi ziti ndipo kufunika kwake ndikotani?

Mayankho:

1. _____________________________________________________

_______________________________________________________

2. _____________________________________________________

________________________________________________________

3. _____________________________________________________

_______________________________________________________

4. _____________________________________________________

_______________________________________________________

V. Tsiku latchitatu anauka kwa akufa.

1. Werengani za kuuka kwa Yesu mu Yohane 20.

2. Werengani za m'mene Apositoli Paulo amanenera za kuuka kwa akufa mu Akorinto 15.

3. Werengani za m'mene Akhrisitu adzakhalire ndi moyo mwa M'khrisitu.

4. Werengani za mphoto yakupulumitsidwa m'mene Paulo anenera mu Akolose 3:1-4.

Mafunso:

1. Kodi Yesu anantsonyedza bwanji kuti anali ndi mphamvu zogonjetsa imfa?

2. Kodi M'khrisitu angakhale bwanji atauka mwa akufa?

3. Popeza anthu onse kudzera mu machimo amangoganizira za kugahena, Vesi 5 likuthathauza chiyani kwa inu?

4. Mwa anthu onse pa dziko lapansi ndichifukwa chiyani Akhrisitu ayenera kukhala achitsangalaro?

Mayankho:

1. _____________________________________________________

_______________________________________________________

2. _____________________________________________________

________________________________________________________

3. _____________________________________________________

_______________________________________________________

4. _____________________________________________________

_______________________________________________________

VI. Anapita kumwamba, nakakhala kudzanja lamanja la Mulungu Atate waphamvu zonse.

1. Werengani nkhani yopita kumwamba m'mene iliri mu Macitidwe a Apositoli ndime 1:1-11.

2. Werengani kuti Yesu ali kumwamba chifukwa cha ife mu

Ahebri 9:24-28.

3. Werengani Ahebri 4:14-16 kuti mudziwe chifukwa chake tili okhadzikika ndikukhala ndi moyo wabwino.

4. Werengani Yohane woyamba 2:1 kuti mumve zimene Yesu akuchita kumwamba.

5. Werengani Aefeso 2:1-9 kuti muone kuti moyo wathu ndi Yesu kumwamba ndi mphoto yapamwamba ndi yamtengo wapatali.

Mafunso:

1. Kodi ndi ubatizo wanji wa mzimu woyera umene Yesu analonjeza ophunzira ake, nanga unafanidziridwa bwanji mu

Macitidwe 2:1-41?

2. Ndi chifukwa chiyani pembedzo limodzi lokha linkakwanira?

3. Ndi chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi chikhulupiliro m'maphephero anthu kwa Mulungu wamphamvu zonse?

4. Kodi kukhala m'khrisitu kumatanthauza kuti sitingachimwe?

5. Ganizirani ndime ya Agalatiya 4:1-7. Kodi kusunga mwambo muulamuliro wamphamvu wonga ngati "Iwe Pita" ndikosabvuta?

Mayankho:

1. _____________________________________________________

____________________________________________________

2. _____________________________________________________

________________________________________________________

3. _____________________________________________________

_______________________________________________________

4. _____________________________________________________

_______________________________________________________

5. _____________________________________________________

_______________________________________________________

VII. Kuchokera kumwamba adzabwera kudzaweruza amoyo ndi akufa.

1. Werengani Afilipi 3 kuti mudziwe cholinga cha m'khrisitu aliyense.

2. Werengani Tito 2 za m'mene m'khrisitu ayenera kukhalira poyembekezera kubwera kwa Yesu.

3. Werengani Atesalonika woyamba 4:13-18 ndime imene imanena za kubwera kwa Yesu.

4. Werengani nthano zimene Yesu ananena mu Mateyu 25.

5. Werengani Atesalonika 1:3-10 kuti muphunzire za chifundo cha Mulungu.

Mafunso:

1. Powerenga vesi 20 kodi M'khrisitu angaganizire bwanji podzindikira kuti Yesu ndi Mlengi, Mpulumutsi, ndi omuweludza wake?

2. Kodi dalitso la chikhulupiliro cha M'khrisitu ndi chiyani?

3. Mu Chibvumbulutso 1:7 onani kusiyana kwa maganizo a onse amene adzaone kubwera kwa Yesu.

4. Kodi zofunikira zina kuti Yesu atipulumutse ndi chiyani?

5. Poti anthu onse ndi ochimwa ndipo ayenera kulangidwa, nanga Akhrisitu angapulumuke bwanji?

Mayankho:

1. _____________________________________________________

____________________________________________________

2. _____________________________________________________

________________________________________________________

3. _____________________________________________________

_______________________________________________________

4. _____________________________________________________

_______________________________________________________

5. _____________________________________________________

_______________________________________________________

VIII. Ndikhulupilira mu M'zimu Woyera.

1. Werenganinso Agalatiya 4:4-7 za m'mene mzimu unatsinthira akapolo atchimo kukhala ana a Mulungu.

2. Werengani Akorinto wachiwiri 1:20-22 za njira za Mulungu kwa ana ake kuti akhalebe ndi chikhulupiliro chawo.

3. Werengani Aefeso 1:13-14 m'mene Mulungu amakwanilitsira zofuna zathu kudzera mu m'zimu woyera.

4. Werengani Petro woyamba 1:1-2 m'mene Mulungu atsakhira ake.

Mafunso:

1. Kodi M'khrisitu amapulumutsidwa kuchokera kuti? Nanga angapulumutsidwire kuti?

2. Tikawerenga Masalimo 1. Kodi M'khrisitu ayenera kuchita chiyani pazofuna za mzimu woyera?

3. Kodi mzimu woyera umatithandiza ife bwanji panopa ndi ku moyo wosatha?

4. Kodi Aroma 8:18-27 amanena bwanji za mzimu woyera m'mene umapulumutsira anthu osakhidwa?

Maynakho:

1. _____________________________________________________

_______________________________________________________

2. _____________________________________________________

________________________________________________________

3. _____________________________________________________

_______________________________________________________

4. _____________________________________________________

_______________________________________________________

IX. Ndikhulupilira tchalichi cha akatolika oyera, ndichigwirizano cha angelo.

1. Werengani Genesesi 10 m'mene alotereza za tchalichi cha Akatolika kapena kunena kuti tchalichi cha anthu onse.

2. Werengani Macitidwe 10 m'mene mungaphunzire kuti Yesu ndi Mfumu ya mafumu onse ndiponso kuti aliyense angakakhale mu Ulemelero wa Mulungu osati Ayuda okha.

3. Werengani Akorinto woyamba 12 zakuti tchalichi cha Yesu ndi chimodzi koma chiri ndi nthambi zimbiri.

4. Werengani Aefeso 4:1-16 kuti muphuzire za thupi la Khrisitu likulira ndi kukhala ndi chikondi.

Mafunso:

1. Kodi M'chipangano chakale anthu osakhidwa ali ndani?

2. Kodi Genesesi amakwanilitsidwa bwanji mu Macitidwe 10?

3. Kodi mphoto zosiyanasiyana zingatsangalatse bwanji m'chiyanjano cha angelo ku ulemero wa Mulungu?

4. Kodi m'chifukwa chiyani umodzi mu thupi la Khrisitu ndi wofunikira kwambiri ngati cholinga cha M'khrisitu aliyense ndi kupembeza Mulungu?

Mayankho:

1. _____________________________________________________

_______________________________________________________

2. _____________________________________________________

________________________________________________________

3. _____________________________________________________

_______________________________________________________

4. _____________________________________________________

_______________________________________________________

X. Kukhulukiridwa kwa machimo.

1. Werengani Yohane woyamba 1:7 ndi Yohane woyamba 2:1-2 kuti mudziwe zimene zinachitika pamene Akhrisitu anagwera mu machimo.

2. Werengani Aroma 7:21-25 kuti olo m'Khrisitu wopulumutsidwa ayenera kugonjetsa machimo a padziko lapansi.

3. Werengani Aroma 3:21-28, Agalatiya 2:15-16 ndi Ahebri 11 m'mene timaphunzira kuti timayesedwa kudzera m'chikhulupiliro cha chisomo cha Mulungu osati m'chifuniro chathu.

4. Werengani Mika 7:18-19 kuti mumve m'mene chikhulukiliro chathu chinayanjatsilidwa Yesu asanabadwe.

Mafunso:

1. Kodi tingapulumitsidwe bwanji?

2. Chifukwa chiyani m'Khrisitu aliyense ayenera kupepha kukhululukilidwa kwa machimo tsiku liri lonse?

3. Ndi m'njira yotani machimo amachoka mwa munthu wochimwa ngati ine ndi kukhala m'Khrisitu wopanda tchimo?

4. Kodi muganiza bwanji za chigwirzano cha chipangano chakale ndi chatsopano?

Mayankho:

1. _____________________________________________________

____________________________________________________

2. _____________________________________________________

________________________________________________________

3. _____________________________________________________

_______________________________________________________

4. _____________________________________________________

_______________________________________________________

5. _____________________________________________________

_______________________________________________________

XI. Kuuka kwa akufa.

1. Werengani Luka 16:19-31 m'mene Yesu ananenera zina za moyo wosatha.

2. Werengani Afilipi 1:21-24 kuti mudziwe m'mene Paulo anaganidzira za moyo ndi imfa.

3. Werengani Chibvulutso 20:11-15 kuti muone m'mene tidzaweluzidwire.

4. Werengani Yohane woyamba 3:1-3 zakusiyana kokhala m'Khrisitu ndio kusakhala m'Khrisitu.

5. Werengani Akorinto woyamba 2:6-9 kuti umdziwe za zimene anankhozela m'Khrisitu aliyense.

Mafunso:

1. M'mene nthano yi ikunenera kodi tidzakhala ndi chifundo kapena chisoni ndi anzathu okonda za dziko lapansi?

2. Kodi m'khrisitu nagachite chiyani kuti asiye kukonda moyo wa dziko lapansi ndi kukalowa ku moyo wosatha?

3. Werengani Masalimo 139. Kodi timakhala ndi mtendere kapena dadaulo podziwa kuti Mulungu amadziwa maganiza ndi zochita zathu.

4. Chifukwa chiyani anthu ena samalapa machimo awo ndi kubwera kwa Yesu kuti awakhululukire?

5. Kodi ulemelero wakumwamba ndikukhala ndi Mulungu?

Mayankho:

1. _____________________________________________________

_______________________________________________________

2. _____________________________________________________

________________________________________________________

3. _____________________________________________________

_______________________________________________________

4. _____________________________________________________

_______________________________________________________

XII. Ndikukhala ndi moyo wosatha. Amen.

1. Werengani Akorinto wachiwiri 5:1-6 kuti mumve za nyumba yathu ya kumwamba.

2. Werengani Chibvumbulutso 22 ndipo mumalingaliro anu onse muone zimene anatikhozera.

3. Werengani Mateyu 6:9-13 m'mene Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kupephera.

4. Werengani Akorinto wachiwiri 1:18-20 ndi

Chibvumbulutso 22:21-22 za m'mene liwu loti "Amen" limagwiritsilidwa ntchito.

Mafunso:

1. Kodi moyo wathu ndi wokonda dziko lapansi ndi katundu?

2. Kodi ganizo ndi chinthunzi cha nyumba yathu ya kumwamba chimatithandiza bwanji za moyo wathu wa padziko lapansi?

3. Muphephero lomwe Yesu anaphunzitsa, analangiza kuti Dzina la Atate lilemekedzedwe ndi zofuna zake zichitike zimakuthandizani kuona za nyumba ya Atate kumwamba?

4. Poti Ame pachiyambi ankatathauza Choonadi, Kukhulupilika, ndi chiyembekezo, nanga umboni wa Yohane mu Cibvumbulutso ndi wotani kwa ife nanga umatithandiza bwanji?

Mayankho:

1. _____________________________________________________

_______________________________________________________

2. _____________________________________________________

________________________________________________________

3. _____________________________________________________

_______________________________________________________

4. _____________________________________________________

_______________________________________________________

Cholinga

Cholinga cha bukhuli ndikuthandiza anthu kuti aphunzire Baibulo pamodzi. Mu Mateyu 18:19-20 Yesu anati, "ndinenanso, ngati awiri a inu mugwirizana pa zofuna zanu, Atate akumwamba azakuchitirani. Poti ndimakhala pomwe pali anthu awiri kapena atatu mudzina langa."

Muli ololedwa kulemba bukuli kachiwiri. Ngati mufuna kulemba mchinenero china, chonde lemberani kwa: Les Hendricks, c/o Christian Hope Association, 205 South BC Avenue, Suite #105, Lynden WA 98264, USA. Tizakuthandizani kulemba bukhuli kwa ulere. Tiyeni "Aliyense wa ife aphunzitse mzake" chikhale cholinga chathu ndipo "Ulemelero wa Mulungu" ukhale chofuna chathu.

Choncho . . .

Mwamaliza kuphunzira mau a Mulungu, mungathe kuziyetsa nokha? Kodi ubwenzi wanu ndi Yesu Khrisitu ndi wotani? Ngati m'mene Timoteo wachiwiri 3:14-17 alembera zakufunikira kwa mau a Mulungu mu njira zosiyanasiyana, koma Yakobo amanenanso kuti kudziwa mau a Mulungu kokha sikutathauza chipulumutso.

Kuti munthu akhale mwana wa Mulungu, ayenera kuchita ndi kudziwa izi:

1. Kudziwa zotsatira za machimo. Werengani Luka 18:9-14; Samueli wachiwiri ndime 11 ndi 12:1-13; Aroma 3:10-12.

2. Kulandira chipulumutso. Werengani Aefeso 2:1-9; Mariko 16:16; Yohane 20:24-28.

3. Kufalitsa uthenga ndi ntchito zabwino. Werengani Mateyu 10:32-33; Luka 23:39-43; Yakobo 2:26; Yesaya 6:8.

Werengani ndi kuganizira mozama za mau ndi ndimezi ndipo pepherani polapa machimo, ndikupepha Yesu kuti akhale mpulumutsi ndi mtsogoleri wa moyo wanu.